Bishop Mwakhwawa at St Kizito Chigoneka Parish

Bishop Mwakhwawa athokoza a St. Patricks Missionary Society

Arkidayosizi ya mpingo wa Katolika ya Lilongwe yathokonza chipani cha mu mpingo cha St. Patricks kamba ka ntchito zake zomwe chimagwira mu Arkidayosiziyi.

Ambuye othandiza a Arkidayosiziyi, ambuye Vincent Mwakhwawa ndiwo ayankhula izi la mulungu pa 17 March 2024, pambuyo potsogolera mwambo wa nsembe ya Misa yokondwelera chaka cha St. Patricks ku Parish ya St. Kizito, Chigoneka.

Bishop Vincent Mwakhwawa at Chigoneka Parish on St Patrick's Day

Mmawu awo, ambuye Mwakhwawa ati chipanichi chikugwira ntchito yotamandika yotukula anthu ku thupi ndi mzimu mu Arkidayosiziyi komanso dziko lino la Malawi.

Mwazina, ambuye Mwakhwawa ati chipani cha St. Patricks chakhala chikuthandiza mpingo kuno Ku Malawi monga kusula ansembe ku ma seminale, kumanga zipatala, sukulu ndi zina zambiri.
M’mawu awo, bambo mfumu a parishi ya St. Kizito – Chigoneka, bambo Martin Mulholland ati chipanichi chimakhala ndi chidwi pofalitsa uthenga wabwino ngati momwe ankachitira nkhoswe yawo (Patricks Woyera) ndi cholinga chofuna kufikira anthu ochuluka.

Bishop Mwakhwawa at St Kizito Chigoneka Parish
Irish Ambassador to Malawi Séamus O’Grady, Bishop Vincent Mwakhwawa and Parish Priest Fr Martin Mulholland

Chipani cha St. Patricks Missionary Society chimapezeka ku St. Kizito – Chigoneka Parish, Maria Mthandizi wa Akhristu – Mtandire Parish komanso Mtengo wa Nthenga Parish mu Arkidayosizi ya Lilongwe.

Wolemba ndi Edwin Sitima, Radio Alinafe