World Womens Day of Prayer 2025

World Women Day of Prayer 2025

Chaka ndi chaka amayi a Chigoneka zone Area 47 amatenga nawo mbali pa mapemphero a amai pa dziko lonse la pansi. Chaka chino mapempherowa anachitikira ku St Kizito Parish Loweruka pa 22 March. Mutu wamnsonkhano unachokera pa Masalimo 139:14 NDINAKUPANGA IWE MODABWITSA.

World Womens Day of Prayer 2025 at St Kizito Parish Chigoneka

Guests at World Womens Day of Prayer 2025 at St Kizito Parish Chigoneka

Jouyous moment at World Womens Day of Prayer 2025 at St Kizito Parish Chigoneka

Chipembedzo cha tsikulo chinabwera kuchokera ku gulu la mayi achikhristu ochokera ku Cook Islands ku Pacific. Kia Orana ndi mawu a m’chiyankhulo cha Chimaori chimene anthu a Cook Islands amagwiritsira ntchito popatsana moni. Malonjewa amathanthauzanso ‘Mukhale ndi moyo wautali’, ‘mukhale ndi moyo wabwino’, ‘Muwale ngati dzuwa’ komanso ‘Mutha kuvina ndi mafunde’.

Mrs Tammy Phiri
Mrs Tammy Phiri

 

Mlendo wolemekezeka pa mapempherowa anali Mai Tammy Phiri.

Polankhulapo za mapempherowa, Mai Annualita Matope, omwe ali Chairperson wa Catholic Women Association (CWA) pa St Kizito Parish, anati mnsonkhanowo unali wabwino chifukwa amayi anathokoza mulungu chifukwa chowalenga modabwitsa.

World Womens Day of Prayer 2025 at St Kizito Parish Chigoneka

World Womens Day of Prayer 2025 at St Kizito Parish Chigoneka

Mu Chigoneka zone Area 47 muli mipingo iyi: St Kizito Catholic Parish , Kaninga CCAP, Area 47 Assemblies of God, Christ Citadel, Anglican ndi CCAP Livingstonia Synod.